Salimo 135:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Chilichonse chimene Yehova anafuna kuchita anachita.+Anachita zimenezi kumwamba, padziko lapansi, m’nyanja ndi m’madzi onse akuya.+ Yesaya 46:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi.+ Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.+ Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalira zanga zidzachitikadi,+ ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+ Danieli 4:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Iye amaona anthu onse okhala padziko lapansi ngati opanda pake+ ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake pakati pa makamu akumwamba ndi pakati pa anthu okhala padziko lapansi.+ Palibe aliyense amene angaletse dzanja+ lake kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+ Aroma 9:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Mwina unganene kwa ine kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu akupezabe anthu zifukwa? Kodi ndani angatsutse chifuniro chake chimene chinanenedwa?”+
6 Chilichonse chimene Yehova anafuna kuchita anachita.+Anachita zimenezi kumwamba, padziko lapansi, m’nyanja ndi m’madzi onse akuya.+
10 Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi.+ Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.+ Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalira zanga zidzachitikadi,+ ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+
35 Iye amaona anthu onse okhala padziko lapansi ngati opanda pake+ ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake pakati pa makamu akumwamba ndi pakati pa anthu okhala padziko lapansi.+ Palibe aliyense amene angaletse dzanja+ lake kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+
19 Mwina unganene kwa ine kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu akupezabe anthu zifukwa? Kodi ndani angatsutse chifuniro chake chimene chinanenedwa?”+