1 Mbiri 22:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Yehova akupatse nzeru ndi kuzindikira.+ Akupatsenso lamulo lotsogolera Isiraeli, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.+ Yobu 32:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ndithudi, mzimu wa anthuNdiponso mpweya wa Wamphamvuyonse n’zimene zimawachititsa kumvetsa zinthu.+ Salimo 119:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Ndiyendetseni m’njira ya malamulo anu,+Pakuti ndikukondwera ndi njira imeneyi.+ Mlaliki 12:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.
12 Yehova akupatse nzeru ndi kuzindikira.+ Akupatsenso lamulo lotsogolera Isiraeli, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.+
8 Ndithudi, mzimu wa anthuNdiponso mpweya wa Wamphamvuyonse n’zimene zimawachititsa kumvetsa zinthu.+
13 Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.