13 Iwe sunayenera kulowa pachipata cha anthu anga pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.+ Ndithu iweyo sunayenera kuyang’anitsitsa tsoka la m’bale wako pa tsiku limene anawonongedwa. Ndipo sunayeneranso kutambasula dzanja lako ndi kutenga chuma chake pa tsiku limene iye anakumana ndi tsoka.+