Salimo 33:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pakuti iye ananena, ndipo zinachitika.+Iye analamula, ndipo zinakhalapo.+ Salimo 68:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Yehova wapereka lamulo,+Ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.+ Salimo 107:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Iye ananena mawu ndipo anawachiritsa,+Moti anawapulumutsa kudzenje la manda.+