Deuteronomo 8:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Mungaiwale amene anakudyetsani mana+ m’chipululu, chakudya chimene makolo anu sanachidziwe, pofuna kukuphunzitsani kudzichepetsa+ ndi kuti akuyeseni kuti potsirizira pake akuchitireni zabwino.+ Deuteronomo 32:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Akanakhala anzeru,+ akanaganizira mozama zimenezi.+Akanalingalira kuti ziwathera bwanji.+ Salimo 90:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Tisonyezeni mmene tingawerengere masiku athu+Kuti tikhale ndi mtima wanzeru.+ Aheberi 12:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Zoonadi, palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa.+ Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere,+ chomwe ndi chilungamo.+
16 Mungaiwale amene anakudyetsani mana+ m’chipululu, chakudya chimene makolo anu sanachidziwe, pofuna kukuphunzitsani kudzichepetsa+ ndi kuti akuyeseni kuti potsirizira pake akuchitireni zabwino.+
11 Zoonadi, palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa.+ Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere,+ chomwe ndi chilungamo.+