17 Inu Mulungu wanga, ine ndikudziwa bwino kuti inu ndinu wosanthula mitima,+ ndiponso kuti mumakonda chilungamo.+ Ineyo kumbali yanga, ndapereka zinthu zonsezi mwaufulu ndi mtima wowongoka. Ndasangalala kuona anthu anu ali apawa, akupereka zopereka zawo mwaufulu kwa inu.