Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 10:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Tsopano Aisiraeli inu, kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani,+ koposa kuopa+ Yehova Mulungu wanu kuti muziyenda m’njira zake zonse,+ kukonda+ ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,+

  • Miyambo 21:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Kuchita zinthu zoyenera ndi zachilungamo kumamusangalatsa kwambiri Yehova, kuposa kupereka nsembe.+

  • Yesaya 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Phunzirani kuchita zabwino.+ Funafunani chilungamo.+ Dzudzulani munthu wopondereza ena.+ Weruzani mwachilungamo mwana wamasiye.*+ Thandizani mkazi wamasiye pa mlandu wake.”+

  • Yeremiya 22:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova wanena kuti: “Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo, muzilanditsa munthu amene anthu achinyengo akufuna kumulanda katundu wake. Musachitire nkhanza mlendo aliyense wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye* kapena mkazi wamasiye.+ Musawachitire zachiwawa.+ Musakhetse magazi a munthu aliyense wosalakwa m’dziko lino.+

  • Ezekieli 45:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatopa nanu inu atsogoleri a Isiraeli!’+

      “‘Siyani ziwawa ndi kulanda zinthu za anthu anga.+ Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Lekani kulanda zinthu za anthu anga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

  • Hoseya 12:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Koma iwe ubwerere kwa Mulungu wako.+ Usonyeze kukoma mtima kosatha+ ndi chilungamo+ ndipo nthawi zonse uziyembekezera Mulungu wako.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena