Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 19:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musamakondere munthu wosauka,+ ndiponso musamakondere munthu wolemera.+ Mnzako uzimuweruza mwachilungamo.

  • Deuteronomo 16:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Mudziikire oweruza+ ndi atsogoleri+ m’mizinda yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, malinga ndi mafuko anu. Oweruza ndi atsogoleriwo aziweruza anthu ndi chiweruzo cholungama.

  • Yesaya 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Phunzirani kuchita zabwino.+ Funafunani chilungamo.+ Dzudzulani munthu wopondereza ena.+ Weruzani mwachilungamo mwana wamasiye.*+ Thandizani mkazi wamasiye pa mlandu wake.”+

  • Yeremiya 21:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Inu a m’nyumba ya Davide,+ Yehova wanena kuti: “M’mawa uliwonse+ muziweruza mwachilungamo,+ ndipo muzilanditsa munthu kwa anthu achinyengo amene akufuna kumulanda katundu.+ Muzitero kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto+ ndi kukutenthani popanda wouzimitsa chifukwa cha kuipa kwa zochita zanu.”’+

  • Ezekieli 22:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Anthu anyoza abambo ndi amayi awo mwa iwe.+ Mlendo wokhala mwa iwe amuchitira zinthu mwachinyengo.+ Azunza mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.”’”+

  • Ezekieli 22:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Anthu a m’dzikolo abera anthu pochita zachinyengo+ ndiponso zauchifwamba.+ Iwo akuzunza anthu osautsika ndi osauka.+ Abera mlendo pochita zachinyengo komanso zopanda chilungamo.’+

  • Mika 2:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iwo alakalaka minda ya anthu ena ndipo ailanda.+ Alakalakanso nyumba za anthu ena n’kuzitenga kukhala zawo.+ Atenga mwachinyengo cholowa cha munthu ndi cha banja lake.+

  • Zekariya 7:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Muzichita chilungamo chenicheni poweruza milandu.+ Muzisonyezana kukoma mtima kosatha+ ndi chifundo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena