4 Chitani mdulidwe wa mitima yanu pamaso pa Yehova,+ inu anthu a ku Yuda ndi okhala mu Yerusalemu. Chitani zimenezi kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto, pakuti ukatero udzayaka popanda munthu wozimitsa, chifukwa cha zochita zanu zoipa.”+
18 Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+ Moto wa mkwiyo wake udzanyeketsa dziko lonse lapansi,+ chifukwa iye adzafafaniza anthu onse okhala padziko lapansi.”+