Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 10:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Mitima yanu muichite mdulidwe+ ndipo musakhalenso ouma khosi.+

  • Deuteronomo 30:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Yehova Mulungu wanu adzachita mdulidwe wa mitima yanu+ ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.+

  • Yeremiya 9:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ndidzaimba mlandu Iguputo,+ Yuda,+ Edomu,+ ana aamuna a Amoni+ ndi Mowabu+ ndi onse odulira ndevu zawo zam’mbali amene amakhala m’chipululu.+ Pakuti mitundu yonse ndi yosadulidwa ndipo anthu onse a m’nyumba ya Isiraeli sanachite mdulidwe wa mitima yawo.”+

  • Machitidwe 7:51
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 “Anthu okanika inu ndi osachita mdulidwe wa mumtima+ ndi m’makutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mmene anachitira makolo anu inunso mukuchita chimodzimodzi.+

  • Aroma 2:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Koma Myuda ndi amene ali wotero mkati,+ ndipo mdulidwe wake ndi wa mumtima+ wochitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.+ Munthu woteroyo satamandidwa+ ndi anthu koma ndi Mulungu.+

  • Akolose 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Popeza muli naye pa ubwenzi,+ mwadulidwa,+ osati ndi manja a anthu koma mwa kuvula thupi lauchimo,+ chifukwa mdulidwe wa atumiki a Khristu umakhala wotero.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena