Ekisodo 20:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako+ kuti masiku ako atalike m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+ Miyambo 10:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Mwana wozindikira amatuta m’chilimwe. Mwana wochititsa manyazi amakhala ali m’tulo tofa nato pa nthawi yokolola.+ Miyambo 17:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Wantchito wochita zinthu mozindikira, adzalamulira mwana wa mbuye wake amene amachita zinthu zochititsa manyazi,+ ndipo adzalandira nawo cholowa pamodzi ndi ana a mbuye wake.+
12 “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako+ kuti masiku ako atalike m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+
5 Mwana wozindikira amatuta m’chilimwe. Mwana wochititsa manyazi amakhala ali m’tulo tofa nato pa nthawi yokolola.+
2 Wantchito wochita zinthu mozindikira, adzalamulira mwana wa mbuye wake amene amachita zinthu zochititsa manyazi,+ ndipo adzalandira nawo cholowa pamodzi ndi ana a mbuye wake.+