Deuteronomo 19:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 “Usasunthe zizindikiro za malire a mnzako,+ makolo anu ataika kale malire a cholowa chimene udzalandira, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti ulitenge kukhala lako. Deuteronomo 27:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 “‘Wotembereredwa ndi munthu wosuntha chizindikiro cha malire a mnzake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) Yobu 24:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Pali anthu amene amasuntha malire,+Iwo alanda gulu la ziweto kuti aziziweta. Hoseya 5:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Akalonga a Yuda akhala ngati anthu osuntha malire.+ Ndidzawakhuthulira mkwiyo wanga ngati madzi.
14 “Usasunthe zizindikiro za malire a mnzako,+ makolo anu ataika kale malire a cholowa chimene udzalandira, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti ulitenge kukhala lako.
17 “‘Wotembereredwa ndi munthu wosuntha chizindikiro cha malire a mnzake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)