29 “Zinthu zobisika+ ndi za Yehova Mulungu wathu, koma zinthu zoululidwa+ ndi zathu ndi ana athu mpaka kalekale, kuti titsatire mawu onse a chilamulo ichi.+
33 Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri.+ Nzeru+ zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.+ Ziweruzo zake ndi zosasanthulika,+ ndipo ndani angatulukire njira zake?