Miyambo 20:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Usamakonde tulo kuti ungasauke.+ Tsegula maso ako kuti ukhale ndi zakudya zambiri.+ Miyambo 24:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Ukati, “Ndigoneko pang’ono, ndibeko katulo pang’ono, ndipindeko manja pang’ono pogona,”+ Miyambo 26:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Munthu waulesi amapisa dzanja lake m’mbale yodyera, koma amalephera kulibweretsa pakamwa pake chifukwa amaona kuti n’zotopetsa kwambiri.+ Mlaliki 4:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Wopusa amapinda manja+ ake ndipo amadziwononga yekha.+
15 Munthu waulesi amapisa dzanja lake m’mbale yodyera, koma amalephera kulibweretsa pakamwa pake chifukwa amaona kuti n’zotopetsa kwambiri.+