Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 33:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Koma Yakobo anati: “Monga mukudziwa mbuyanga, anawa ndi osakhwima, komanso ndili ndi nkhosa ndi ng’ombe zoyamwitsa.+ Tikaziyendetsa mofulumira kwambiri, ngakhale tsiku limodzi lokha, ndithu zifa zonse.+

  • Ekisodo 23:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Uzigwira ntchito masiku 6.+ Koma tsiku la 7 usamagwire ntchito, kuti ng’ombe yako ndi bulu wako zizipuma, ndipo mwana wa kapolo wako wamkazi ndi mlendo azipumula.+

  • Deuteronomo 22:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Ukaona bulu wa m’bale wako kapena ng’ombe yake itagwa pamsewu usailekerere. Uzim’thandiza m’bale wako mwa kuidzutsa.+

  • Deuteronomo 22:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Usamange ng’ombe ndi bulu kuti uzilimitse pamodzi.+

  • Deuteronomo 25:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.+

  • Yona 4:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Kodi ine sindikuyenera kumvera chisoni mzinda waukulu wa Nineve,+ mmene muli anthu oposa 120,000, omwe sadziwa kusiyanitsa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere? Kodi sindiyenera kumveranso chisoni ziweto zambiri zimene zili mmenemo?”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena