11 Pamenepo anthu onse ndi akulu amene anali pachipata anayankha kuti: “Ndife mboni! Yehova adalitse mkazi amene akulowa m’nyumba mwako kuti akhale ngati Rakele+ ndi Leya,+ akazi amene anabereka ana a nyumba ya Isiraeli.+ Uonetse kulemekezeka kwako mu Efurata+ ndi kudzipangira dzina m’Betelehemu.+