12 Sonkhanitsani anthu,+ amuna, akazi, ana ndi alendo okhala m’mizinda yanu, kuti amvetsere ndi kuphunzira,+ pakuti ayenera kuopa Yehova Mulungu wanu+ ndi kutsatira mosamala mawu onse a m’chilamulo ichi.
11 Koma anthu a ku Bereya anali a mtima wofuna kuphunzira kuposa a ku Tesalonika aja. Iwowa analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri, ndipo tsiku ndi tsiku anali kufufuza+ Malemba+ mosamala kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona.+