Yobu 9:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Ndikudziwa bwino kuti zili choncho.Koma kodi munthu angakhale bwanji wosalakwa pa mlandu wotsutsana ndi Mulungu?+ Yobu 9:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Pakuti iye si munthu+ ngati ine kuti ndimuyankhe,Kapena kuti tizengane mlandu. Yesaya 45:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Tsoka kwa amene walimbana ndi amene anamuumba,+ ngati phale limene likulimbana ndi mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo+ lingafunse amene akuliumba kuti: “Kodi ukupanga chiyani?” Ndipo kodi chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”? Aroma 9:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Munthu iwe!+ Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chinganene kwa munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji motere?”+
2 “Ndikudziwa bwino kuti zili choncho.Koma kodi munthu angakhale bwanji wosalakwa pa mlandu wotsutsana ndi Mulungu?+
9 Tsoka kwa amene walimbana ndi amene anamuumba,+ ngati phale limene likulimbana ndi mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo+ lingafunse amene akuliumba kuti: “Kodi ukupanga chiyani?” Ndipo kodi chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”?
20 Munthu iwe!+ Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chinganene kwa munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji motere?”+