25 Ayuda+ ndi Aisiraeli anapitiriza kukhala mwabata.+ Aliyense anali pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu,+ kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba,+ masiku onse a Solomo.
11 “Solomo anali ndi munda wa mpesa+ ku Baala-hamoni. Munda wa mpesawo anaupereka kwa anthu oti aziusamalira.+ Munthu aliyense anali kubweretsa ndalama zasiliva zokwana 1,000 zolipirira zipatso za mundawo.