20Chotero ana onse a Isiraeli anatuluka,+ kuchokera ku Dani+ mpaka kumunsi ku Beere-seba,+ ndipo khamu lonselo linasonkhana pamodzi mogwirizana+ kwa Yehova ku Mizipa,+ pamodzinso ndi anthu a m’dera la Giliyadi.+
11 Ndiye ine malangizo anga ndi onena kuti: Sonkhanitsa ndithu Isiraeli yense pamaso pako kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba.+ Akhale ochuluka ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja,+ ndipo iweyo uwatsogolere kunkhondo.+
15 Pamenepo Yehova anagwetsa mliri+ mu Isiraeli kuyambira m’mawa mpaka nthawi yoikidwiratu, moti pa anthu onse kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba+ panafa anthu 70,000.+