9 Wachititsa mtima wanga kugunda, iwe mlongo wanga,+ mkwatibwi wanga.+ Wachititsa mtima wanga kugunda ndi diso lako limodzi lokha,+ ndiponso ndi diso limodzi lokha la mkanda wa m’khosi mwako.
4 Khosi lako+ lili ngati nsanja ya mnyanga wa njovu. Maso ako+ ali ngati maiwe a ku Hesiboni,+ amene ali pafupi ndi chipata cha Bati-rabimu. Mphuno yako ili ngati nsanja ya Lebanoni, imene inayang’ana cha ku Damasiko.