10 Anthu owomboledwa ndi Yehova adzabwerera+ n’kukafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Iwo azidzasangalala mpaka kalekale.+ Adzakhala okondwa ndi osangalala ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+
17 chifukwa Mwanawankhosa,+ amene ali pambali pa mpando wachifumu, adzawaweta+ ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi+ a moyo. Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.”+