22 Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni.+ Kumeneko anapezako Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ mbadwa za Anaki.*+ Mzinda wa Heburoni+ unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani+ wa ku Iguputo usanamangidwe.
11 Akalonga a ku Zowani+ ndi opusa ndithu. Malangizo a anthu anzeru ochokera pakati pa alangizi a Farao, ndi osathandiza.+ Kodi anthu inu mudzamuuza bwanji Farao kuti: “Ine ndine mwana wa anthu anzeru, mwana wa mafumu akale”?