-
Nehemiya 12:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Ndiyeno mwambo wotsegulira+ mpanda wa Yerusalemu uli pafupi kuchitika, anthu anafunafuna Alevi m’malo awo onse ndi kubwera nawo ku Yerusalemu. Anachita izi kuti potsegulira mpandawo pakhale kusangalala ndi kuyamika+ Mulungu mwa kuimba nyimbo+ pogwiritsa ntchito zinganga, zoimbira za zingwe+ ndi azeze.+
-
-
Yesaya 61:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 ndiponso kuti anthu onse amene akulirira Ziyoni ndiwapatse nsalu yovala kumutu m’malo mwa phulusa,+ ndiwapatse mafuta kuti azisangalala+ m’malo molira, ndiwapatse chovala choti azivala ponditamanda m’malo mokhala otaya mtima.+ Iwo adzatchedwa mitengo ikuluikulu ya chilungamo,+ yobzalidwa ndi Yehova+ kuti iyeyo akongole.+
-