7 Ngakhale dokowe, mbalame youluka m’mlengalenga, imadziwa bwino nthawi yake yoikidwiratu.+ Ndipo njiwa,+ namzeze ndi pumbwa, iliyonse mwa mbalame zimenezi imadziwa nyengo yobwerera kumene yachokera. Koma anthu anga sakudziwa chiweruzo cha Yehova.”’+