29 Ndiwe wodala Isiraeli iwe!+
Ndani angafanane ndi iwe,+
Anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova,+
Chishango chako chokuthandiza,+
Amenenso ndi lupanga lako lopambana?+
Adani ako adzakhala mwamantha chifukwa cha iwe,+
Ndipo iwe udzayendayenda pamalo awo okwezeka.”+