17 M’zigawo zonse ndi m’mizinda yonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake linafika, Ayuda anali kusangalala ndi kukondwera. Anachita phwando+ ndipo linali tsiku lachisangalalo. Anthu ambiri+ a m’dzikomo anayamba kudzitcha Ayuda+ chifukwa anali kuchita mantha kwambiri+ ndi Ayudawo.