-
Yesaya 43:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Mitundu yonse isonkhanitsidwe pamalo amodzi, ndipo mitundu ya anthu ikhale pamodzi.+ Ndani pakati pawo amene anganene zimenezi?+ Kapena ndani amene angatiuze zinthu zimene zidzayambirire kuchitika?+ Abweretse mboni zawo+ kuti akhale olungama ndipo mbonizo zimve ndi kunena kuti, ‘Zimenezo ndi zoona!’”+
-
-
Yesaya 45:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Lankhulani ndipo mufotokoze mlandu wanu.+ Inde, iwo afunsanefunsane mogwirizana. Kodi ndani wachititsa zimenezi kuti zimveke kuyambira kalekale?+ Ndani wazinena kuyambira nthawi imene ija?+ Kodi si ine Yehova, amene palibenso Mulungu wina kupatulapo ine?+ Ine ndine Mulungu wolungama ndi Mpulumutsi+ ndipo palibenso wina kupatulapo ine.+
-