Yesaya 2:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 M’tsiku limenelo, munthu wochokera kufumbi adzataya milungu yake yasiliva yopanda pake ndi milungu yake yagolide yopanda phindu, imene anthu anamupangira kuti aziigwadira. Adzaitayira kumene kumakhala aswiswiri* ndi mileme,+ Yesaya 45:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+ Yeremiya 10:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+
20 M’tsiku limenelo, munthu wochokera kufumbi adzataya milungu yake yasiliva yopanda pake ndi milungu yake yagolide yopanda phindu, imene anthu anamupangira kuti aziigwadira. Adzaitayira kumene kumakhala aswiswiri* ndi mileme,+
20 “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+
5 Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+