Yeremiya 6:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 “Kodi ndilankhule ndi ndani ndipo ndichenjeze ndani kuti amve? Taonani! Makutu awo sanawachite mdulidwe, moti sangamve.+ Taonani! Mawu a Yehova akhala onyozeka kwa iwo,+ ndipo sakukondwera nawo.+ Zekariya 7:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Koma iwo anakanabe kumvetsera.+ Anapitiriza kumulozetsa nkhongo+ ndipo anatseka makutu awo kuti asamve chilichonse.+ Yohane 3:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Amene amachita zinthu zoipa+ amadana ndi kuwala ndipo safika pamene pali kuwala, kuti ntchito zake zisadzudzulidwe.+ Machitidwe 28:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Pakuti anthu awa aumitsa mtima wawo, ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Iwo atseka maso awo, kuti asaone ndi maso awo, asamve ndi makutu awo ndi kuti asazindikire ndi mtima wawo n’kutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”’+
10 “Kodi ndilankhule ndi ndani ndipo ndichenjeze ndani kuti amve? Taonani! Makutu awo sanawachite mdulidwe, moti sangamve.+ Taonani! Mawu a Yehova akhala onyozeka kwa iwo,+ ndipo sakukondwera nawo.+
11 Koma iwo anakanabe kumvetsera.+ Anapitiriza kumulozetsa nkhongo+ ndipo anatseka makutu awo kuti asamve chilichonse.+
20 Amene amachita zinthu zoipa+ amadana ndi kuwala ndipo safika pamene pali kuwala, kuti ntchito zake zisadzudzulidwe.+
27 Pakuti anthu awa aumitsa mtima wawo, ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Iwo atseka maso awo, kuti asaone ndi maso awo, asamve ndi makutu awo ndi kuti asazindikire ndi mtima wawo n’kutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”’+