-
Levitiko 5:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 “Munthu akachita mosakhulupirika mwa kuchimwira zinthu zopatulika za Yehova+ mosadziwa, pamenepo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yake ya kupalamula.+ Nkhosayo mtengo wake uzikhala masekeli* asiliva+ ofanana ndi sekeli la kumalo oyera* kuti ikhale nsembe ya kupalamula.
-
-
Numeri 6:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ndipo apereke kwa Yehova nsembe ya iye mwini. Nsembeyo ikhale nkhosa yaing’ono yamphongo yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yopsereza.+ Aperekenso mwana wa nkhosa wamkazi wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yamachimo.+ Komanso apereke nkhosa yamphongo yopanda chilema, monga nsembe yachiyanjano.+
-