13 Panthaka ya anthu anga, pakungomera zitsamba zaminga.+ Zamera panyumba zonse zimene kale zinali zodzaza ndi chisangalalo. Zamera m’tauni imene kale inali yodzaza ndi chikondwerero.+
26 Ndinayang’anitsitsa ndipo ndinaona kuti munda wa zipatso unali utasanduka thengo. Mizinda yake yonse inali itagwetsedwa.+ Zimenezi zinachitika ndi dzanja la Yehova chifukwa cha mkwiyo wake woyaka moto.