20“Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, musachite nawo mantha mukaona kuti ali ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo,+ ndiponso mukaona kuti adani anuwo ndi ochuluka kwambiri kuposa inu. Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ali ndi inu.+
4 Ana okondedwa, inu ndinu ochokera kwa Mulungu, ndipo mwagonjetsa anthu amenewo,+ chifukwa amene muli ogwirizana+ naye ndi wamkulu+ kuposa amene ali wogwirizana ndi dziko.+