Ekisodo 13:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Chotero Mose anauza anthuwo kuti: “Muzikumbukira tsiku lino limene munatuluka mu Iguputo,+ m’nyumba ya ukapolo, chifukwa Yehova anakutulutsani mmenemo ndi mphamvu ya dzanja lake.+ Choncho musadye chilichonse chokhala ndi chofufumitsa.+ Deuteronomo 3:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Amuna inu, musawaope amenewo, chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye akukumenyerani nkhondo.’+ Deuteronomo 31:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Limbani mtima ndipo chitani zinthu mwamphamvu.+ Musawaope kapena kuchita nawo mantha,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono.”+ Salimo 20:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ena akunena za magaleta* ndipo ena akunena za mahatchi,*+Koma ife tidzanena za dzina la Yehova Mulungu wathu.+ Salimo 46:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Yehova wa makamu ali ndi ife.+Mulungu wa Yakobo ndiye malo athu okwezeka ndiponso achitetezo.+ [Seʹlah.] Miyambo 21:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Hatchi* anaikonzera tsiku la nkhondo,+ koma Yehova ndiye amapulumutsa.+ Aroma 8:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Ndiye tinene kuti chiyani pa zinthu zimenezi? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+
3 Chotero Mose anauza anthuwo kuti: “Muzikumbukira tsiku lino limene munatuluka mu Iguputo,+ m’nyumba ya ukapolo, chifukwa Yehova anakutulutsani mmenemo ndi mphamvu ya dzanja lake.+ Choncho musadye chilichonse chokhala ndi chofufumitsa.+
6 Limbani mtima ndipo chitani zinthu mwamphamvu.+ Musawaope kapena kuchita nawo mantha,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono.”+
7 Ena akunena za magaleta* ndipo ena akunena za mahatchi,*+Koma ife tidzanena za dzina la Yehova Mulungu wathu.+
7 Yehova wa makamu ali ndi ife.+Mulungu wa Yakobo ndiye malo athu okwezeka ndiponso achitetezo.+ [Seʹlah.]
31 Ndiye tinene kuti chiyani pa zinthu zimenezi? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+