7 “‘Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa m’nyumba imeneyi.+ Ine ndidzadzaza nyumbayi ndi ulemerero,’+ watero Yehova wa makamu.
15 N’chifukwa chake ali pamaso+ pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika+ usana ndi usiku m’kachisi wake, ndipo wokhala pampando wachifumuyo+ adzatambasulira hema+ wake pamwamba pawo kuti awateteze.