-
Yesaya 30:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Uwu ndi uthenga wokhudza zilombo zokhala kum’mwera:+ Podutsa m’dziko lamavuto+ ndi la zowawa, la mikango ndi kulira kwa akambuku, la mphiri ndi la njoka zothamanga zaululu wamoto,+ iwo anyamulira chuma chawo pamsana pa abulu akuluakulu.+ Anyamuliranso katundu wawo pamalinunda a ngamila. Koma zinthu zimenezi zidzakhala zopanda phindu kwa anthu amenewa.
-