17 Ndi ndalama zimenezi, ukagule mwamsangamsanga ng’ombe zamphongo,+ nkhosa zamphongo,+ ana a nkhosa amphongo,+ limodzi ndi nsembe zake zambewu+ ndiponso nsembe zake zachakumwa.+ Zimenezi ukazipereke paguwa lansembe la panyumba ya Mulungu wako,+ yomwe ili ku Yerusalemu.+