9 Mawu onsewa anthu adzawadziwa.+ Efuraimu ndi anthu okhala ku Samariya,+ adzawadziwa mawuwo chifukwa cha kudzikweza kwawo ndiponso chifukwa cha mwano wa mumtima mwawo. Pakuti iwo anena kuti:+
4 Palibe chimene mudzachite, koma mudzagwada pakati pa akaidi ndiponso muzidzagwa pakati pa anthu amene aphedwa.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+