19 Ndipo ine ndinali ngati mwana wa nkhosa wamphongo wokondedwa mwapadera, amene akupita kukaphedwa.+ Ine sindinadziwe kuti andikonzera ziwembu+ ndi kunena kuti: “Tiyeni tiwononge mtengowu pamodzi ndi zipatso zake. Tiyeni timuchotse m’dziko la anthu amoyo,+ kuti dzina lake lisakumbukikenso.”