5 Ukuloseranso kuti, ‘Mfumu ya Babulo idzatenga Zedekiya kupita naye ku Babulo ndipo adzakhala komweko kufikira nditamucheukira,’+ watero Yehova. Ukunenanso kuti, ‘ngakhale kuti anthu inu mukupitiriza kumenyana ndi Akasidi simudzapambana.’ N’chifukwa chiyani ukulosera zimenezi?”+