14 Sipadzapezeka aliyense wothawa kapena wopulumuka mwa otsala a Yuda amene alowa m’dziko la Iguputo ndi kukhala mmenemo monga alendo,+ kupatulapo anthu ochepa chabe amene adzathawa. Sipadzapezeka wobwerera kudziko la Yuda kumene akulakalaka kubwerera kuti akakhaleko.’”+