8 “‘“‘Ndiyeno mtundu uliwonse wa anthu ndi ufumu umene sudzatumikira Nebukadinezara mfumu ya Babulo, umenenso sudzaika khosi lake m’goli la mfumu ya Babulo, ine ndidzaulanga ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri+ kufikira nditaufafaniza kudzera mwa Nebukadinezara,’+ watero Yehova.