9 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+
12 Ndiyeno m’mwezi wachisanu, pa tsiku la 10 la mweziwo, m’chaka cha 19 cha ulamuliro wa Mfumu Nebukadirezara+ ya Babulo, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali kutumikira mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu.