33 Kenako Farao Neko+ anamanga+ Yehoahazi ku Ribila+ m’dziko la Hamati, kuti asalamulirenso ku Yerusalemu. Ndiyeno Farao Neko analamula+ dzikolo kuti lim’patse matalente 100 a siliva+ ndi talente imodzi ya golide.+
5 Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linawathamangitsa+ ndipo Zedekiya anamupeza m’chipululu cha Yeriko.+ Atamugwira, anamutenga ndi kupita naye kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ku Ribila,+ m’dziko la Hamati,+ kuti Nebukadirezara akamuweruze.+