29 Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu abwera kudzayatsa moto mzindawu kuti upseretu.+ Ayatsanso nyumba zawo chifukwa pamadenga ake amafukizirapo nsembe zautsi kwa Baala ndipo amathira nsembe zachakumwa kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.’+