36 Kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli m’mbali mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso kuchokera kumzinda wa m’chigwa mpaka ku Giliyadi, panalibe mzinda womwe unali wa malinga aatali kwambiri kwa ife.+ Yehova Mulungu wathu anawapereka onsewo kwa ife.
5 Kenako anawoloka Yorodano ndi kumanga msasa ku Aroweli+ kudzanja lamanja la mzinda umene uli pakati pa chigwa,* kuyang’ana kudziko la Agadi+ ndi ku Yazeri.+
8 ndi Bela. Bela anali mwana wa Azazi, Azazi anali mwana wa Sema, Sema anali mwana wa Yoweli.+ Bela anali kukhala m’dera loyambira ku Aroweli+ mpaka kukafika ku Nebo+ ndi ku Baala-meoni.+