10 Ndidzathetsa phokoso lachikondwerero ndi phokoso lakusangalala m’malowo.+ Ndidzathetsanso mawu osangalala a mkwati ndi a mkwatibwi.+ Simudzamvekanso kupera kwa mphero+ ndipo simudzaonekanso kuwala kwa nyale.+
12 Kukondwera kwachoka pamaso pa ana a anthu.+ Ndithu mtengo wa mpesa wauma ndiponso mtengo wa mkuyu wafota. Mtengo wa makangaza* komanso mtengo wa kanjedza, mtengo wa maapozi ndi mitengo yonse yakuthengo yauma.+