18 Nyumba ya Yakobo idzakhala ngati moto,+ nyumba ya Yosefe idzakhala ngati malawi a moto ndipo nyumba ya Esau idzakhala ngati mapesi.+ Motowo udzayatsa mapesiwo ndi kuwanyeketsa. Sipadzakhala wopulumuka aliyense wa nyumba ya Esau,+ pakuti Yehova mwiniyo wanena.