16 Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera.+ Pakuti chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu,+ Yerusalemu ndi anthu anu takhala chinthu chotonzedwa ndi anthu onse otizungulira.+