Masalimo
91 Aliyense wokhala m’malo otetezeka+ a Wam’mwambamwamba+
Adzakhala wosungika mumthunzi wa Wamphamvuyonse.+
2 Ndidzauza Yehova kuti: “Inu ndinu pothawirapo panga ndi malo anga achitetezo,+
Mulungu wanga amene ndimamukhulupirira.”+
4 Adzakutchinjiriza ndi mapiko ake,+
Udzathawira pansi pa mapiko ake.+
Choonadi chake+ chidzakhala chishango chako+ chachikulu ndi malo ako achitetezo.
5 Usiku sudzaopa choopsa chilichonse,+
Ndipo sudzaopanso muvi+ woponyedwa masana,
6 Sudzaopa mliri umene umayenda mu mdima,+
Kapena chiwonongeko chimene chimachitika dzuwa lili paliwombo.+
7 Anthu 1,000 adzagwa pambali pako,
Ndipo anthu 10,000 adzagwa kudzanja lako lamanja.
Koma palibe zoterezi zimene zidzakuchitikira.+
9 Popeza wanena kuti: “Yehova ndiye pothawirapo panga,”+
Wapanga Wam’mwambamwamba kukhala malo ako okhalamo.+
10 Palibe tsoka limene lidzakugwera,+
Ndipo ngakhale mliri sudzayandikira hema wako.+
13 Udzapondaponda mkango wamphamvu ndi njoka ya mamba,+
Ndipo udzapondaponda mkango wamphamvu kwambiri ndi chinjoka.+
14 Mulungu wanena kuti: “Popeza wasonyeza kuti amandikonda,+
Inenso ndidzamupulumutsa.+
Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa.+